[Script Info] Title: [Events] Format: Layer, Start, End, Style, Name, MarginL, MarginR, MarginV, Effect, Text Dialogue: 0,0:00:01.45,0:00:04.20,Default,,0000,0000,0000,,Pamene aneneri ndi aphunzitsi \Na tchalitchi chakale Dialogue: 0,0:00:04.20,0:00:07.93,Default,,0000,0000,0000,,anali kusala kudya ndi kupemphera, \NMzimu Woyera unauza Paulo ndi Baranaba Dialogue: 0,0:00:07.93,0:00:10.09,Default,,0000,0000,0000,,kuti ayende ulendo woyamba wa umishonale. Dialogue: 0,0:00:10.09,0:00:13.38,Default,,0000,0000,0000,,Tchalitchi chinawapempherera asananyamuke \Nulendo wawowo. Dialogue: 0,0:00:15.76,0:00:19.15,Default,,0000,0000,0000,,Iwo anaikidwa manja, ndipo tinawapempherera \Nmochokera pansi pa mtima. Dialogue: 0,0:00:19.15,0:00:22.17,Default,,0000,0000,0000,,Monga tchalitchi chogwirizana, \Ntinawapempherera kuti ayende bwino Dialogue: 0,0:00:22.17,0:00:24.36,Default,,0000,0000,0000,,ndiponso kuti Mulungu awapatse \Nmawu oyenerera Dialogue: 0,0:00:24.36,0:00:25.89,Default,,0000,0000,0000,,oti akayankhule kwa anthu ambirimbiri. Dialogue: 0,0:00:25.89,0:00:28.64,Default,,0000,0000,0000,,Tinapempherera amishonale athuwa kuti \Nzinthu ziwayendere bwino Dialogue: 0,0:00:28.64,0:00:31.24,Default,,0000,0000,0000,,pantchito yawo yofalitsa uthenga wabwino. Dialogue: 0,0:00:32.28,0:00:34.66,Default,,0000,0000,0000,,Paulo ndi Baranaba anayenda kupita \Nkumadera osiyanasiyana. Dialogue: 0,0:00:34.66,0:00:38.48,Default,,0000,0000,0000,,Ku Kupro, analalikira mawu a Mulungu \Nm'masunagoge a Ayuda. Dialogue: 0,0:00:38.48,0:00:41.79,Default,,0000,0000,0000,,Ku Antiyokeya wa ku Pisidiya, pafupifupi \Nanthu onse mumzindawo anasonkhana Dialogue: 0,0:00:41.79,0:00:43.79,Default,,0000,0000,0000,,kuti adzamve mawu a Ambuye. Dialogue: 0,0:00:43.79,0:00:46.34,Default,,0000,0000,0000,,Anthu Amitundu atamva uthenga \Nwawo, anakhulupirira. Dialogue: 0,0:00:46.34,0:00:49.57,Default,,0000,0000,0000,,Mawu a Ambuye anafalikira \Nm'chigawo chonse, Dialogue: 0,0:00:49.57,0:00:53.93,Default,,0000,0000,0000,,ndipo ophunzira anali kusangalala kwambiri \Nkomanso anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. Dialogue: 0,0:00:56.34,0:00:58.98,Default,,0000,0000,0000,,Paulo ndi Baranaba anaika akulu \Nmu tchalitchi chilichonse Dialogue: 0,0:00:58.98,0:01:02.33,Default,,0000,0000,0000,,ndipo ankasala kudya ndi kuwapempherera \Npowapereka kwa Ambuye. Dialogue: 0,0:01:02.33,0:01:05.22,Default,,0000,0000,0000,,Iwo anasonkhanitsa tchalitchi chonse \Npamodzi n'kuwauza Dialogue: 0,0:01:05.22,0:01:07.22,Default,,0000,0000,0000,,zonse zimene Mulungu anachita \Nkudzera mwa iwowo Dialogue: 0,0:01:07.22,0:01:10.43,Default,,0000,0000,0000,,ndiponso mmene anatsegulira khomo la \Nchikhulupiriro kwa anthu Amitundu.