Pamene aneneri ndi aphunzitsi
a tchalitchi chakale
anali kusala kudya ndi kupemphera,
Mzimu Woyera unauza Paulo ndi Baranaba
kuti ayende ulendo woyamba wa umishonale.
Tchalitchi chinawapempherera asananyamuke
ulendo wawowo.
Iwo anaikidwa manja, ndipo tinawapempherera
mochokera pansi pa mtima.
Monga tchalitchi chogwirizana,
tinawapempherera kuti ayende bwino
ndiponso kuti Mulungu awapatse
mawu oyenerera
oti akayankhule kwa anthu ambirimbiri.
Tinapempherera amishonale athuwa kuti
zinthu ziwayendere bwino
pantchito yawo yofalitsa uthenga wabwino.
Paulo ndi Baranaba anayenda kupita
kumadera osiyanasiyana.
Ku Kupro, analalikira mawu a Mulungu
m'masunagoge a Ayuda.
Ku Antiyokeya wa ku Pisidiya, pafupifupi
anthu onse mumzindawo anasonkhana
kuti adzamve mawu a Ambuye.
Anthu Amitundu atamva uthenga
wawo, anakhulupirira.
Mawu a Ambuye anafalikira
m'chigawo chonse,
ndipo ophunzira anali kusangalala kwambiri
komanso anadzazidwa ndi Mzimu Woyera.
Paulo ndi Baranaba anaika akulu
mu tchalitchi chilichonse
ndipo ankasala kudya ndi kuwapempherera
powapereka kwa Ambuye.
Iwo anasonkhanitsa tchalitchi chonse
pamodzi n'kuwauza
zonse zimene Mulungu anachita
kudzera mwa iwowo
ndiponso mmene anatsegulira khomo la
chikhulupiriro kwa anthu Amitundu.