WEBVTT 00:00:02.000 --> 00:00:04.200 Pamene aneneri ndi aphunzitsi a tchalitchi chakale 00:00:04.200 --> 00:00:07.930 anali kusala kudya ndi kupemphera, Mzimu Woyera unauza Paulo ndi Baranaba 00:00:07.930 --> 00:00:10.090 kuti ayende ulendo woyamba wa umishonale. 00:00:10.090 --> 00:00:13.180 Tchalitchi chinawapempherera asananyamuke ulendo wawowo. 00:00:15.620 --> 00:00:18.620 Iwo anaikidwa manja, ndipo tinawapempherera mochokera pansi pa mtima. 00:00:18.620 --> 00:00:21.370 Monga tchalitchi chogwirizana, tinawapempherera kuti ayende bwino 00:00:21.370 --> 00:00:23.730 ndiponso kuti Mulungu awapatse mawu oyenerera 00:00:23.730 --> 00:00:25.730 oti akayankhule kwa anthu ambirimbiri. 00:00:25.730 --> 00:00:28.050 Tinapempherera amishonale athuwa kuti zinthu ziwayendere bwino 00:00:28.050 --> 00:00:30.280 pantchito yawo yofalitsa uthenga wabwino. 00:00:32.280 --> 00:00:34.660 Paulo ndi Baranaba anayenda kupita kumadera osiyanasiyana. 00:00:34.660 --> 00:00:38.480 Ku Kupro, analalikira mawu a Mulungu m'masunagoge a Ayuda. 00:00:38.480 --> 00:00:41.790 Ku Antiyokeya wa ku Pisidiya, pafupifupi anthu onse mumzindawo anasonkhana 00:00:41.790 --> 00:00:43.790 kuti adzamve mawu a Ambuye. 00:00:43.790 --> 00:00:46.340 Anthu Amitundu atamva uthenga wawo, anakhulupirira. 00:00:46.340 --> 00:00:49.570 Mawu a Ambuye anafalikira m'chigawo chonse, 00:00:49.570 --> 00:00:53.240 ndipo ophunzira anali kusangalala kwambiri komanso anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. 00:00:56.340 --> 00:00:58.980 Paulo ndi Baranaba anaika akulu mu tchalitchi chilichonse 00:00:58.980 --> 00:01:02.330 ndipo ankasala kudya ndi kuwapempherera powapereka kwa Ambuye. 00:01:02.330 --> 00:01:05.220 Iwo anasonkhanitsa tchalitchi chonse pamodzi n'kuwauza 00:01:05.220 --> 00:01:07.220 zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwowo 00:01:07.220 --> 00:01:10.430 ndiponso mmene anatsegulira khomo la chikhulupiriro kwa anthu Amitundu.