[Script Info] Title: [Events] Format: Layer, Start, End, Style, Name, MarginL, MarginR, MarginV, Effect, Text Dialogue: 0,0:00:02.00,0:00:04.20,Default,,0000,0000,0000,,Pamene aneneri ndi aphunzitsi a tchalitchi chakale Dialogue: 0,0:00:04.20,0:00:07.93,Default,,0000,0000,0000,,anali kusala kudya ndi kupemphera, Mzimu Woyera unauza Paulo ndi Baranaba Dialogue: 0,0:00:07.93,0:00:10.09,Default,,0000,0000,0000,,kuti ayende ulendo woyamba wa umishonale. Dialogue: 0,0:00:10.09,0:00:13.18,Default,,0000,0000,0000,,Tchalitchi chinawapempherera asananyamuke ulendo wawowo. Dialogue: 0,0:00:15.62,0:00:18.62,Default,,0000,0000,0000,,Iwo anaikidwa manja, ndipo tinawapempherera mochokera pansi pa mtima. Dialogue: 0,0:00:18.62,0:00:21.37,Default,,0000,0000,0000,,Monga tchalitchi chogwirizana, tinawapempherera kuti ayende bwino Dialogue: 0,0:00:21.37,0:00:23.73,Default,,0000,0000,0000,,ndiponso kuti Mulungu awapatse mawu oyenerera Dialogue: 0,0:00:23.73,0:00:25.73,Default,,0000,0000,0000,,oti akayankhule kwa anthu ambirimbiri. Dialogue: 0,0:00:25.73,0:00:28.05,Default,,0000,0000,0000,,Tinapempherera amishonale athuwa kuti zinthu ziwayendere bwino Dialogue: 0,0:00:28.05,0:00:30.28,Default,,0000,0000,0000,,pantchito yawo yofalitsa uthenga wabwino. Dialogue: 0,0:00:32.28,0:00:34.66,Default,,0000,0000,0000,,Paulo ndi Baranaba anayenda kupita kumadera osiyanasiyana. Dialogue: 0,0:00:34.66,0:00:38.48,Default,,0000,0000,0000,,Ku Kupro, analalikira mawu a Mulungu m'masunagoge a Ayuda. Dialogue: 0,0:00:38.48,0:00:41.79,Default,,0000,0000,0000,,Ku Antiyokeya wa ku Pisidiya, pafupifupi anthu onse mumzindawo anasonkhana Dialogue: 0,0:00:41.79,0:00:43.79,Default,,0000,0000,0000,,kuti adzamve mawu a Ambuye. Dialogue: 0,0:00:43.79,0:00:46.34,Default,,0000,0000,0000,,Anthu Amitundu atamva uthenga wawo, anakhulupirira. Dialogue: 0,0:00:46.34,0:00:49.57,Default,,0000,0000,0000,,Mawu a Ambuye anafalikira m'chigawo chonse, Dialogue: 0,0:00:49.57,0:00:53.24,Default,,0000,0000,0000,,ndipo ophunzira anali kusangalala kwambiri komanso anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. Dialogue: 0,0:00:56.34,0:00:58.98,Default,,0000,0000,0000,,Paulo ndi Baranaba anaika akulu mu tchalitchi chilichonse Dialogue: 0,0:00:58.98,0:01:02.33,Default,,0000,0000,0000,,ndipo ankasala kudya ndi kuwapempherera powapereka kwa Ambuye. Dialogue: 0,0:01:02.33,0:01:05.22,Default,,0000,0000,0000,,Iwo anasonkhanitsa tchalitchi chonse pamodzi n'kuwauza Dialogue: 0,0:01:05.22,0:01:07.22,Default,,0000,0000,0000,,zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwowo Dialogue: 0,0:01:07.22,0:01:10.43,Default,,0000,0000,0000,,ndiponso mmene anatsegulira khomo la chikhulupiriro kwa anthu Amitundu.