0:00:02.000,0:00:04.200 Pamene aneneri ndi aphunzitsi a tchalitchi chakale 0:00:04.200,0:00:07.930 anali kusala kudya ndi kupemphera, Mzimu Woyera unauza Paulo ndi Baranaba 0:00:07.930,0:00:10.090 kuti ayende ulendo woyamba wa umishonale. 0:00:10.090,0:00:13.180 Tchalitchi chinawapempherera asananyamuke ulendo wawowo. 0:00:15.620,0:00:18.620 Iwo anaikidwa manja, ndipo tinawapempherera mochokera pansi pa mtima. 0:00:18.620,0:00:21.370 Monga tchalitchi chogwirizana, tinawapempherera kuti ayende bwino 0:00:21.370,0:00:23.730 ndiponso kuti Mulungu awapatse mawu oyenerera 0:00:23.730,0:00:25.730 oti akayankhule kwa anthu ambirimbiri. 0:00:25.730,0:00:28.050 Tinapempherera amishonale athuwa kuti zinthu ziwayendere bwino 0:00:28.050,0:00:30.280 pantchito yawo yofalitsa uthenga wabwino. 0:00:32.280,0:00:34.660 Paulo ndi Baranaba anayenda kupita kumadera osiyanasiyana. 0:00:34.660,0:00:38.480 Ku Kupro, analalikira mawu a Mulungu m'masunagoge a Ayuda. 0:00:38.480,0:00:41.790 Ku Antiyokeya wa ku Pisidiya, pafupifupi anthu onse mumzindawo anasonkhana 0:00:41.790,0:00:43.790 kuti adzamve mawu a Ambuye. 0:00:43.790,0:00:46.340 Anthu Amitundu atamva uthenga wawo, anakhulupirira. 0:00:46.340,0:00:49.570 Mawu a Ambuye anafalikira m'chigawo chonse, 0:00:49.570,0:00:53.240 ndipo ophunzira anali kusangalala kwambiri komanso anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. 0:00:56.340,0:00:58.980 Paulo ndi Baranaba anaika akulu mu tchalitchi chilichonse 0:00:58.980,0:01:02.330 ndipo ankasala kudya ndi kuwapempherera powapereka kwa Ambuye. 0:01:02.330,0:01:05.220 Iwo anasonkhanitsa tchalitchi chonse pamodzi n'kuwauza 0:01:05.220,0:01:07.220 zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwowo 0:01:07.220,0:01:10.430 ndiponso mmene anatsegulira khomo la chikhulupiriro kwa anthu Amitundu.